19/09/2026
Dziwani zambiri za 3rdWorld Xplorations ndi Xpeditions 2030.
3rdWorld Xplorations ndi bizinesi yaying'ono yomwe ikufuna kukhazikitsidwa kuti izithandizira ntchito za kafukufuku kudzera m’malonda ang'onoang'ono.
Cholinga chake chachikulu ndi chofuna kuyankha mafunso akulu-akulu okhuzana ndi dziko lapansi ndi moyo wa munthu (philosophical and anthropological questions). Makamaka, kufuna kudziwa ngati ndizotheka dziko la pansi kukhala lokomera tonse (the true nature of our world and the possibilities of its transformation into a better living place for all).
Choncho Xpeditions 2030 ndi ulendo osunga mbiri ya zochitika m'moyo wa tsiku-ndi-tsiku m'Malawi ndi kuyeselera njira zogwiritsa ntchito zipangizo zachilengedwe-zalokolo munjira zawukadawulo zosafuna ndalama zambiri. Kufuna kudziwa ngati ndizothekadi aliyense kupeza zinthu zofunikira mosavuta, ndikuzichotsera usiwa patokha (an equitable, just and livable futuristic world).
Komabe, zikuwonetsa kuti ndizovuta kwambiri chifukwa anthu ambirife timawona kuti usiwa ndi omwe umatithandiza kupeza zolandira kapena umphawi wa dziko umatithandiza kupeza chuma mobisa.
Anthu ambiri timawona ngati palibenso njira ina kuposa kupempha, kuba mwam'chinunu kapena kuphatikiza ukamberembere pochita zinthu zopezera ndalama. Timati "nanga titani? ndi m'mene timadyera" (survivalistic livelihood). Komanso timati "bola zanga zindiyendere" (opportunistic livelihood).
Timatenga zochitika zofuna kuthetsa umphawi (za chitukuko kapena zamabungwe) ngati njira yopezera zolandira kapena chuma chabe, timati "kulembetsa" kapena kuti "kuchitola/kuyiphula". Njira zenizeni zothetsera umphawi wa dziko timaziwona zinthu zolakwika kwambiri (monga kuthetsa katangale ndi kudalira zolandira, komanso kupeza njira zawukadawulo (research & innovating)).
Chifukwa chakuti mu Xpeditions 2030 palibe kuzimbayitsa, kusinjilira kapena kuphsyatira, zofooka zathu zimawonekera patali. Choncho, ulendowu siwokomera anthu ambiri. Chonde, tisatsatire ngati tikuziwona zosagwirizana kapena zophwanyitsa mutu.