12/07/2026
Zoona Za Kusamalira Nkhumba Kufika 90kg Mu Miyezi 5
Alimi atsopano ambiri a nkhumba amaona zithunzi ndi makanema pa intaneti a nkhumba zomwe zimafika 90kg mu miyezi 5 yokha, ndipo nthawi yomweyo amaganiza kuti ndi muyezo wamba.Chifukwa chake pamene nkhumba zawo zili ndi 60–70kg pa msinkhu womwewo, amayamba kudera nkhawa kapena kuganiza kuti pali vuto.
Koma zoona zake ndi izi:Inde, nkhumba zingafike 90kg mu miyezi 5, koma sizichitika mwangozi, ndipo sizichitika pa famu iliyonse.Zinthu zambiri zimakhudza mmene nkhumba zimakula, ndipo ngati chimodzi chikusowa, kukula kumachedwa.
Genetics (mbewu):Nkhumba yokhala ndi mbewu yabwino imakula mofulumira komanso imagwiritsa ntchito chakudya bwino kuposa yokhala ndi mbewu zoipa, ngakhale zonse zili pa chakudya chimodzi.
Zakudya (nutrition):Kukula mofulumira kumafuna chakudya chokwanira chokhala ndi mphamvu, mapuloteni, mavitamini ndi mchere. Kupereka chakudya chochuluka chokha sikutanthauza kuti nkhumba zikula mwachangu ngati chakudyacho sichili choyezeka bwino.
Kasamalidwe (management):Nkhumba zimakula bwino zikakhala ndi madzi oyera nthawi zonse, malo okwanira odyera, khola loyera komanso losangalatsa, komanso kusowa kwa kupsinjika. Kuchulukitsa nkhumba m’khola, mpweya wosakwanira, ndi kusapereka chakudya nthawi zonse zimachepetsa kukula.
Zaumoyo (health):Tizilombo ta m'mimba, matenda, kapena ngakhale mavuto ang’ono omwe sakuwoneka bwino amatha kuchepetsa kukula ndi mmene nkhumba zimagwiritsa ntchito chakudya.
Kusiyana kwa nkhumba:Osaiwala kuti nkhumba sizimakula mofanana. Ngakhale zomwe zimachokera mu nthumba imodzi zingachite bwino mosiyana.
Cholakwika chimene alimi atsopano amachita ndi kufunafuna nambala yokha osayang’ana zinthu zomwe zimabweretsa nambalayo.Ngati nkhumba zako zili ndi thanzi, zikukula mosalekeza, komanso zikugwiritsa ntchito chakudya bwino, ndiye kuti uli pa njira yoyenera kale.Kuyesera kukakamiza kukula mwachangu kudzera mu chakudya chochulukitsa kapena njira zachangu zosafunika nthawi zambiri kumawonjezera mtengo wa chakudya osapereka zotsatira zabwino.
Pamene maziko ali bwino, nkhumba zako zimachita bwino kwambiri kufika pa mphamvu ya mbewu zawo.Kumbukirani: cholinga sichokhala ndi nkhumba zolemera mwachangu, koma kukhala ndi nkhumba zathanzi komanso zopindulitsa.
🔴 Nkhumba zako zimafika kulemera kotani pafupifupi pa miyezi 5, ndipo ndi mtundu wanji umene ukuweta?