29/08/2026
KUSIYA KUYAMWA NDI GAWO LINA LAKUKULA KWABWINO!
Ku Nasindeni Farms timaonetsetsa kuti tiana ta nkhumba takula bwino komanso tili ndi thanzi labwino.
Tima piglets timayamba kutipasa creep feed kwa two weeks tikasiya kuyamwa. Creep feed imeneyi imakhala ndi mapuloteni ambiri (high protein content) komanso zakudya zofunikila kuti tima piglets tiyambe kuzolowera kudya chakudya cholimba.
✨ Ubwino wa creep feed ndi monga
* Imathandiza pa kukula ndi kupanga minofu chifukwa imakhala ndi protein yokwanira.
* Imachepetsa stress yomwe tima piglets amakumana nayo panthawi yosiyidwa kuyamwa.
* Imathandiza kuti tima piglets tipitirize kulemera bwino komanso kukula mwachangu
* Imathandiza kuti m'mimba mwa tima piglets tizolowere zakudya zolimba pang'onopang'ono.
Pa miyezi iwiri, tima piglets tathu timakhala takonzeka kusiya kuyamwa chifukwa cha preparation yabwino
Good feeding. Good management. Better pigs
Nasindeni Farms😊 Raising better pigs, one litter at a time.