11/08/2026
ZAYENKHA ANAVIIKA NSIMA MMADZI?
Bizinesi yanu ndi yaingโono kale, koma mukufuna muitukule nokha. Mumayika ndalama, mumayesetsa kulengeza malonda anu, koma makasitomala sakuchuluka monga momwe mumayembekezera.
Vuto si mankhwala amene akukupangirani kumudzi. ๐ Sikuti njoka zikukawa makasitomala anu ayi! Nthawi zina vuto limakhala lakuti palibe anthu okwanira akulankhula za bizinesi yanu kwa anthu amene angakhale makasitomala anu.
Anthu amene muli nawo pa WhatsApp nawo ayamba kutopa kumva za bizinesi yanu tsiku lililonse. Nawonso ali ndi mabizinesi awo komanso zinthu zina zomwe amakonda komanso kuyangโanira. Choncho, muyenera kufikira anthu atsopano komanso anthu amene ali ndi mwayi wokhala makasitomala anu. kapena kukulumikidzitsani ndi makasitomala ena.
Apa ndi pomwe NETWORKING imakhala yofunika kwambiri. Apa ndi pomwe Anzathu Pamalonda Network imabwela. Apa ndipomwe mukufunika kuti mulowe nawo gulu la nathu ochita malonda anzanu ndikudziwa kuti kodi iwo amapanga chani.
Mukalumikizana ndi anzanu ochita malonda, amatha kuthandiza anthu ena kudziwa za bizinesi yanu. Kudzera mwa anzanuwa, m***a kupeza makasitomala atsopano, ma referral komanso mwayi wina wa bizinesi.
Komanso, networking sikungokuthandizani kupeza makasitomala. Mukakumana ndi anthu ena ochita bizinesi, mumaphunzira kuchokera kwa iwo. M***a kuona momwe akukulitsira mabizinesi awo, zomwe zikuwathandiza komanso zomwe akuphunzira kapena aphunzira mmene akupanga bizinesi.
Mukamakambirana nawo, mumapezanso mwayi wogawana mavuto omwe mukukumana nawo mu bizinesi yanu. Ena mwa anzanuwa mwina anakumanapo kale ndi vuto lomwelo ndipo angakupatseni nzeru kapena njira yomwe ingakuthandizeni kulithetsa.
Choncho, musamangokhala mukuyesetsa kukulitsa bizinesi yanu nokha. Khalami membala wa anzathu pamalonda lero. Lembetsani kuri mukhale membala, ndipo pakali pano kulembetsa ndi ulele.
Kumanani ndi ma volunteers athu ndikulembetsa. Kapena titumidzileni uthenga ku [email protected]. Kapena titumidzileni message pa facebook pompano, or ,kupanga comment tibwela ku inbox kwanu.
Mwayi olembetsa mwaulele ukutha pa 20th August, 2026.
Ziwani kuti anzathu pamalonda network ili mu maboma onse mu malawi muno.