23/09/2025
UBWINO WAMASAMBA ACHAM'MWAMBA KAPENA KUTI MORINGA🌳
```Musabalalike ndimau oti Moringa dzina lanchichewa ndi CHAMMWAMBA ngati simukwadziwa masambawo afunseni anzanu sizimasowa izi```
*1.KUNENEPETSA THUPI.*
✍️Kuyanika masamba aawisi a moringa mum'thudzi ndi kusinja akawuma ndi kusefa. Ufa wakewo umanenepetsa ukamathira m'phala. Ana onyentchera ayenera kumalandira moringa m'phala kuti anenepe.
*2. KUCHOSA MATENDA OSIYANA SIYANA NTHUPI.*
✍️Mukamadya pothira m'phala ufa wake, mudzapewa kutentha thupi, chifukwa cha m'mapapo, matenda a maso ndi m'khutu ndipo yemwe akudwala matenda a HIV/ Aids zimakhala bwino kumadya Moringa chifukwa matenda osiyanasiyana amachepa.
*3. KUWAWA KWA MUTU.*
✍️Kutikita pa chipumi masambawo kumathandiza kuziziritsa mutu komanso potafuna nthangala zitatu za Mulinga kumathandizira kuti mutu uleke kuwawa, matenda a shuga amachepa, zilonda zam'mimba zimatha ndipo chiseyeye chimatha mu usinini.
*4. CHILONDA CHOCHEKEKA*
✍️Ngati mwachekeka sinjani masamba anthete a moringa ndi kumata pochekekapo ndipo matenda ena salowapo komanso sipamatupa.
*5. MATENDA A LINYESU.*
✍️Ngati mwadwala matenda alinyetsu, matani zosinjidwa zija pamalopo.
*6. ZILONDA ZAMMIMBA.*
✍️Tiyi wa masamba a moringa amathandiza kuchotsa zilonda zam'mimba komanso kuthetsa kutsekula kwa m'mimba.
*7. KUSOWA KWA MAGAZI NTHUPI.*
✍️Mu moringa muli 'Iron' wambiri yemwe amathandizira kupanga magazi. Ndiye pachifukwa ichi, odwala onse osowa magazi, amawalimbikitsa kumadya moringa posakaniza zakudya zawo.
*8. KUBWELESA NKAKA MMAWELE*
✍️Amayi oyamwitsa azimwa chakumwa chopangidwa ndi maluwa a moringa powiritsa maluwawo. Mphamvu ya maluwa a moringa imathandizira kupanga mkaka wambiri mwa mayiyo.
*9-KUTETEDZA CHIKHOZODZO*
✍️Chakumwa chomwecho cha maluwa a moringa chimathandiza kuti njira zotulutsira mkodzo zisamakhale ndi matenda.
*10 -KUCHOSA NYONGOLOSI ZAMMIMBA.*
✍️Mukamadya zibalobalo za moringa za nthete,mudzachotsa nyongolotsi
0993500406 sms