Melin Business Consultancy Service

Melin Business Consultancy Service We provide professional business consulting services. Are you a small business owner needing help? Looking for a trusted advisor for strategic insight?

Maybe some Q&A sessions to bounce id

We help entrepreneurs at any stage of their business lifecycle.

28/02/2022

Bambo Ali ndi ana atatu azaka za MMA 15 mpaka 18 ndi mkazi wake,
Watsegula grocery.

Pamene zimalakwika. amalemba wantchito wogulitsa, wina osesa kapena kukolopa mu shop Mwezi ukatha nkumawalipira.

Pamene njira yabwino ndikugwira ndi ana akewa nkumawalipira. Imene awalipirayo ndi imene idzikhalanso pocket money ndiye kuti, mayinso yakumutu ndizina azichotsa pa malipiro awo.

Mwaona kuti apa wapulumutsa ndalamayi chifukwa bwezi akuwapatsabe koma apa akuilandira ngati malipiro, komanso wapulumutsa chakudya, transport ndi zina za wantchito

Business imafunika kuganiza choncho.

12/02/2022

ZIMENE MUNGACHITE KUTI BUSINESS YANU IZIYENDA BWINO.

1. Muzilandira bwino ma kasitomala, anthu ambiri amakonda kugula zinthu Malo amene amalandilidwa bwino, kaya muli ndi shop, kaya mukugulitsa mbewu olo kabaza buziness imene silandira bwino anthu sizimaiyendera bwino.

2. Muziika zinthu zanu pa Malo ochezera ngati Facebook, Whatsapp ndi Zina

3. Muziipatsa Moto, muzipanga zinthu ngati ma Vidiyo, ma Logo, ma poster komanso zithunzi za business yanu , (Ifeyo timapanga zimenezi pa mtengo wazii)

4. Muzikhala ndi cholinga CHOTI mukwanilitse nkumayesetsa kukwanilitsa cholingacho. Mwina mungaike cholinga CHOTI muzilandira bwino ma kasitomala ndiye zimenezi zingakweze business yanu.

5. Muzikhala ndi nthawi yopuma, kumangogwira ntchito osapuma kumapangitsa kuti muzikhala otopa nthawi zonse, simungamaganize bwino, komanso m***a kumadwaldwala zonsezi zingasokoneze business yanu.

6. Muzipempha makasitomala Anu kuti aziuzako ena za inu, iyi ndi njira imene mungapezere makasitomala ambiri.

Lembani Zotsala munsimu.

Chonde Pangani like pageyi komanso muuzeko anzanu kuti apange like kapena muwapange invite. Kuti muzinva zambiri

10/02/2022

Ma business amene mungayambe mu 2022.

1. Kuoda mbewu.
- m***a kuoda mbewu anthu akamakolora kenako nkuzigulitsa pakapita nthawi.

2. Ngati kumene mukukhala anthu ambiri akamanga nyumba m***a kuyamba kuoda cement nkumagulitsa.

3. Ngati Ndalama yanu ndiyambiri komanso ndinu driver m***a kugula galimoto nkumayendera nokha (Mukapatsa anyamata muzidwala mutu daily)

4. M***a kumaoda katundu ku south Africa nkudzagulitsa kuno.

5. M***a kumakaoda Zitenje ku Zambia nkumadzagulitsa kuno.

6. Ngati muli ndi luso lazamanja m***a kuyamba buziness yantchitoyo mmalo modikira kuti wina achitekukulembani ntchito.

7. M***a kumaoda nyama kapena mbewu nkuzigulitsa mmakampani aakulu kapena ma restaurant.

Lembani ma business ena mmusimu.

Pangani like page yathu kuti muzinva zambiri.

03/02/2022

M'MENE MUNGAWERENGELELE PHINDU PA BIZINEZI YANU.

Choyamba dziwani kuti mufunika kulemba zonse zimene mwalowetsa komanso kugwiritsa ntchito pa bizinezi yanu.

1. Lembani ndalama zonse zimene mwalowetsa, mwachitsanzo lembani:

Ndalama yowodera zinthu, K1000
Transport. K50
Waganyu. K5
Chakudya pogulitsa zinthu. K20

NDalama zimenezi ndi zimene mwalowetsa ku bizinezi yanu zonse pamodzi ndi: K1075

Kenako katundu wanu mwagulitsa K1275

Tsopano chotserani Ndalama imene mwapeza K1275 ku K1075 yowodera

PHINDU K200

Malangizo: Ndalama imene mungadye ndi K200. iyo yowodera musaigwire, kupanda apo BIZINEZI YANU itha kugwa.

Pangani like page yathu kuti muzinva zambiri zokhudza business.

02/02/2022

ZOYENERA KUPEWA
MUKAMAYAMBA BUSINESS.

1. Musathere nthawi yambiri Ndikulemba plan, mmalo make muzifufuza zambiri zokhudza businessyo.

2. Musafulumire kulemba anthu ntchito, mpaka patadutsa miyezi ingapo.

3. Ngati ndizotheka ndi mtundu wa business yanu, musafulumire kupanga rent shop kapena office yaikulu muzyamba pang'onopang'ono.

4. Musamaiwale kudzilipira Mwezi ukatha.

5. Musamaiwale kulemba chilichonse chimene mwalowetsa ku business olo itakhala one kwacha.

Pangani like page yathu kuti munve zambiri za business.

02/02/2022

ZOYENERA KUCHITA POYAMBA BIZINEZI

1. Lembani plan ya business yanu.
2. Mukhale ndi mpamba oyambira.
3.Lembetsani bizinezi yanu kuti zitavuta anthu asadzalande katundu wanu.
4. Pezani MRA tin yolipirira mnsonkho. Kuti muzitha kupanga malonda ndi ma company.
5. Pangitsani zithunzi, mavideos komanso ma poster odziwikitsa BIZINEZI yanu.
6. Tsugulani account
7. Dziwani kumene mungapezeko malangizo, ngati kwa maloya, othandiza pa BIZINEZI ngati ifeyo komanso kwa anthu ena.

Izi ndi zimene zingakuthendizeni
Kuyamba BIZINEZI

Pa page yathuyi muzipezapo nkhani zothandizani kuyamba komanso kutukula BIZINEZI yanu chonde panga follow and like page yathu

01/02/2022

Kodi Muli ndi Business koma siikupita patsogolo? Kapena mukufuna kuyamba business koma simukudziwa upangiri wake? Kapena mulibe mpamba? Pangani like page yathu ya pamene tikhale tikufutukula zambiri zokhudza kuyamba business.

01/02/2022

Hello! Do you need a senior business consultant to help you attain your goals or create a business plan? I can help you develop your business growth strategies, budget, team structure, operational objectives and review business documents.

I experience in management consulting, leadership coaching, consumer goods, and manufacturing industries creating business strategy, financial modeling, operational leadership, program management, and defining team structures.

Business consulting expertise

- Starting a business advice
- Create your business plan or sales proposal
- Review or edit your business plan
- Company overview
- Industry overview
- Market analysis (i.e., Sizing; TAM, SAM, SOM)
- Competitive analysis
- Marketing & Sales
- Financial model & funding needs
- Projected Statements: Income, Balance Sheet, Cash Flow
- Help with LivePlan
- proofread and edit of your business plan

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Melin Business Consultancy Service posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share