14/05/2024
ππππ
Admin please undibise osandivula chigobaππ
ndikufuna Anthu athandize kupemphela Ambuye andikhululukile pa zomwe ndinachita Malemu amuna anga, ndinalodza chifukwa choti ndinapeza ali ndi chibwezi chomwe amachipasa ndalama kwinaso amagulila zomvala zodula mkaziyo pomwe ine samandisamala.
nde ine nangoganiza zopeza mankhwala kuwalodza chifuna napsa mtima ndi zomwe amandichita. sinachite kufuna k*ti ndiwamphe koma zomwe amandipangazo ndizomwe zimandiwawa moyo mwanga ona ndinaganiza zoti ndingowamphaπππ. Nde panops saname ndikuvutika kwambili ana ndikukanika kuwasamala ndekha chifukwa shorp yomwe anandisiyila atamwalilayo inaduka zinthu sizimayenda chimwalilileni amuna angawo.
Ndinali maganizo achimwana simadziwa zomwe ndikuchita anali satana yemwe akandinamiza. chifukwa ine mawona ngati akamwalilamo sivutika chifukwa madalila shorp yoo k*ti ndiziyindesa kumapeza thandizo losamalila ana pakhomo.. koma tsoka lake shorp yoo inatha pano kuvutika kuchita kulakalaka amuna anga akanakhala moyo chifukwa simasowa kalikose pakhomo amathandiza, chabe sanje ndiyomwe inandipangisa k*ti ndifike powampha. kusaka maganyu anthu sakundilemba or mamuna oti ndipange naye chibwezi azithandiza akusowa or modzi ondifusila. please admin thandizeni ngati alipo angandipemphelele k*ti ambuye andikhululukile machimo anga ndipo andisungile chisisi ku akwawo amuna anga asadziwe zoti mwana wawo namumpha ndine chifukwa atha kundimpha. mamuna wanga anali munthu yekhayo yomwe kwawoko amadalila ndamene anali ochitikako bwino nde ataziwa zoti ndiwampha ine sangandisiye ndimoyoππ please admin ngatiso pangapezeke mamuna ofuna mkazi ndipangeni naye connect ndipo asandiwone ineyo singazampheso mamuna panopa ndine munthu owopa Mulungu ndipo satana sangandigwilitse ntchito ndikuvutika ine saname π please thandizeni osat kundiweludza ndikumafika paja pofuna kuzimangilila k*ti satile amuna anga koma ndikuwopa k*ti ana anga asowa owasamala. please help me ndasowa mtengo ogwila π
Follow nice page ππ» MR TK