23/03/2021
MICHAEL USI ( MANGANYA)
Dr Michael Bizwick Usi yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Manganya anabadwa m'chaka cha 1968 mumzinda wa Bulawayo ku Zimbabwe. Michael ndi wachiwiri kubadwa m'banja la ana atatu,anyamata okaokha. Iye anabadwa mapasa ndi Clever yemwe anatisiya zaka zingapo zapitazo. Woyamba kubadwa ndi Bizwick,mchimwene wake. Bambo ake a Michael ankachokera m'boma la Mulanje,mudzi wotchedwa Golden, mfumu yaikulu Chikumbu pomwe mayi ake anali amtundu wa Ndebele ;ankachokera m'mudzi wa Nkayi, mfumu yaikulu Makiriwa m'dziko la Zimbabwe.
Ngakhale anabadwira ku Zimbabwe, Michael anakulira ku Mulanje ndikuyambanso sukulu ku Mulanje konko. Iye anachita maphunziro ake apulaimale pa Mulanje LEA Primary School kuchokera sitandade 1 mpaka 8. Atalemba mayeso aboma a sitandade 8,Michael anasankhidwa n'kukachita maphunziro ake asekondale pa sukulu yogonera konko ya Mulanje komwe analemba MSCE yake. Kenako,anakachita maphunziro a diploma in clinical medicine ku Malamulo Medical College n'kuyamba ntchito ngati medical assistant pachipatala cha St Luke's ku Zomba. Nthawi zina,ankathandiziranso kuchipinda chochitira operation.
Atachoka kuntchito ya udotolo, Michael anayamba kugwira ntchito ku Adventist Development and Relief Agency (ADRA) komwe anagwira ntchito kwa zaka zopitilira makumi awiri. Iye anali programs director kubungweli.
Manganya wakhala akuchita zisudzo kwa zaka zochuluka ndipo ndi m'modzi wa atengambali odziwika bwino m'sewero la Tikuferanji lomwe linayambitsidwa ndi iye pansi pabungwe la ADRA. Iyeyu amakondanso kuimba, mwachitsanzo ,anatulutsapo nyimbo yotchedwa 'ngenge'. Amakondanso kumvera nyimbo zachimalawi monga za Malemu Grace Chinga, Ethel Kamwendo Banda, Faith M***a ndi Namadingo.
Padakali pano ,Dr Manga ndi nduna yoona zokopa alendo ndi chikhalidwe. Iyenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani chandale cha UTM.Ngakhale ali nduna,Manganya akupitilizabe kuchita zisudzo;posachedwapa wachita "act" limodzi ndi Mr Jokes mu 'video' yotchedwa Ife ndi Achikhalidwe.
Kupatula maphunziro tatchula aja, Michael alinso ndi maphunziro ena apamwamba. Mwachitsanzo,iye ali ndi PhD yomwe anaipeza kuchokera ku University of Bedfordshire m'dziko la United Kingdom. PhD yake inachita research ya youth engagement in development.
Manganya ndi wokwatira. Iye anamanga banja ndi Ella Mpita yemwe ndi namwino pachipatala cha Blantyre Adventist. Awiriwa ali ndi ana.
LIKE AND FOLLOW OUR PAGE FOR MORE!