27/07/2017
Bambo wina anaona ngati k*tulo atamva mtengo wa ticket ya sitima yomwe amafuna kugula, unali mtengo okwera kwambiri kuposa momwe iye anakonzekera..
Poti unali ulendo ofunika, mosasangalatsidwa anangodula ticket ija nkuika thumba, tsopano nkhawa yake inali yoti akhala ndi njala paulendo onse poti ndalama inathera kugula ticket ija, ndipo anazilimbitsa mtima k*ti bola akafike, iye anati ikafika nthawi yoti anthu akugula zakudya azikangolowa k*toilet...
Ulendo unayambika ndipo amachitadi zomwe anaganiza, akalengeza k*ti ino ndi nthawi yachakudya, iye ndim'mene amakalowa mu toilet, zinachitika katatu konse, tsono atalengesanso k*ti ndi nthawi yazakudya, apapa nk*ti tsono atatsala pang'ono kufika moti kameneko kanali kotsiliza, zitachitikanso zolowa mu toilet, neba wake yemwe anayandikana naye anamufunsa k*ti kodi kuchakudyaku sindikumakuonani mukumakhala k*ti?..
Apapa nk*ti tsono Bamboyu akuoneka ofooka, ndipo anati, ndilibe ndalama iliyonse yogulira zakudya, ndalama zanga zinathera kugula ticket, sindinadziwe k*ti inali yodula chotero, neba wake uja anamufunsa k*ti
"KODI MWAWELENGA ZOMWE ZILI PATICKET YANU"?..
Nkulu uja anavomela ndi mphamvu, komatu neba uja anati taituluseni mutembenuze k*tseliko, atatembenuza anapeza k*ti kwalembedwa Mau oti: "MUKAGULA TICKETI ZAKUDYA NDI ZAULELE"..
Bambo uja sanamvetse, anafunsanso munthu wakumbuyo k*ti: ETI NDIZOONA TICKET YANU YALEMBEDWANSO IZI? ndipo wina uja anavomeladi ndikumutsimikizila k*ti ulendo onse amadya zakudya zaulele...
Izitu nzomwe ife anthu otchedwa asilamu tikuchita, chipulumutso ndi chaulele, koma nthawi zonse pomwe tamva za mau a Allah mpamene tik*thawa kukabisala muutchimo, ticket yapaulendo tinagula kale Quraan tili nalo, koma sitikuwelenga nkudziwa zomwe zalembedwamo, k*tero ambiri anatemedwa mphini thupi lao ati kufuna kudziteteza, ena ak*taya ndalama zambiri mwa asing'anga ati kugula moyo, sadziwa k*ti chofunika ndikukhulupirira Allah ndi mtumiki wake basi. Bambo uja amakabisala mu toilet moipa nkumafa ndi njala zakudya zili zaulele ndipo pamapeto pake analira, ifenso tizalira tikuuzidwa k*ti kupysa tikupysaku nzofuna dala poti chipulumutso ndi chaulele. Tiyeni kuyambila lero tiziwelenga ma Quraan omwe akungoyanga ndi kangaude mma display suitcase ngakhale amene Ali mmafoni mwathumu, komanso timpembedze Allah kasanu patsiku.
Abale anga mchipembedzo tiyeni tiyang'ane kuseli kwa ticket yathu coz chipulumutso ndi chaulele. Allah akudalisen nonse_ kamba kakumvetsera ulaliki umenewu kmanso atipangise ife mimtima yathu k*t tizikhala omukumbukira iye Ameen yaa Allahabad Sangam Nagri