24/05/2026
Boma linathangitsa aMalawi kuti asamakumbe golide mmadera ena adziko lino chifukwa chopanda ma licence, chonsecho ndi boma lomwero limagula golide kwa anthu opanda ziphaso kuzera ku Reserve Bank Of Malawi. Posachedwapa taona boma likugulitsa golide yemweyo ndi cholinga chakuti apeze ndalama zakunja kuti ligulire mafuta. Umu ndimomwe ndinachezera ndi Percy Maleta amene ndi wapampando wankhulu wa bungwe la Federation of Artisanal and Small-Scale Mining in Malawi.
Kodi aMalawi, mukuonapo bwanji pankhani imeneyi? Mwina kapena boma lingowa phunzitsa anthuwa kenako kuwapatsa ziphaso poti ndi boma lomwero likupindura nawo.
Mining Review Malawi
Department of Mining Mw
Natural Resources Justice Network - NRJN
Future Miners Network
Ignatius Kamwanje
Export Development Fund