11/03/2025
IMAGINE UKHALE NDI MPAMBA WA 3 MILLION KWACHA
Business idea 1
Uzipita ku Tanzania kukaoda zinthu za 2.1 million inayo transport ndi zodula zina ndiye ugulitse zonse nkupeza phindu la 4 million kwacha
Business Idea 2
Uode mpunga, nyemba, khobwe, soya ndizanyemba zina konkuno ku Malawi transport 500,000. ugulitse ndikupeza 5 million kwacha
Business idea 3
Ugule sausage making machine uzipanga sausage konkuno ku Malawi ndi ma meatballs amene utamapanga za smart komaso zokoma nkumapanga supply mmashop akuluwa nkupeza 5.5 million kwacha
Business idea 4
Uzipanga bake ma snack abwino uziperekera mmashop komaso kumayendetsa mmisika yomwe utapeza ma partnership abwino utha kumapeza more than 5.5 million kwacha.Iyiyi utha kumapeza ma order okaperekera mma conference ndi mma meeting ena as far as mmapanga zabwino komaso zokoma.
Business idea 5
Uwete nkhuku zamazira or zanyama kapena zinziri.Pazanyama uzigulitsa zamoyo, zokupha kale, chicken parts, kanyenya or take away ntaonjezera chips and ntayamba ndi nkhuku 200 nkumagulitsa 20,000 each
Nanga utapanga zamazira nkumagulitsa maziraso...imagine utamapanga hatch anapiye wekha ndiye uzigulitsaso anapiye.Nkhuku imodzi iziikira 30 eggs uzipanga hatch nkhuku 200 every 21 days nkumagulitsa anapiye and mazira or Zina uzipha pakutha miyezi 6 ukhala ulipati
Uwete zinziri 300 uzipanga hatch mazira uzigulitsa anapiye or mazira omwewo komaso zinzirizo.Pano zitatu ndi 8000-10000.Dzira limodzi la zinziri ndi 500-1500 coz ndimankhwala
Business idea 6
Ulimire mtedza or nyemba.Nyemba pa acre mukazisamala imatha kutulutsa matumba 20 a 50kg.1 kg pano ndi 7000 above tiyerekeze mwapeza 50kg *7000 * 20kg.... zakudimba or zammunda nde ukhale ndi ma acre 4 or 6 from that amount based on location
Business idea 7
Muode ma slip-on ndi nsapato Zina mmashop akuluwa muzikagulitsa mmisika...from 3 million transport 300,000 uthamange mu khilisimasi umu pofika end December upeze 6 million above
Business idea 8
Ugule nkhumba or mbuzi uziphe mu December.Nkhumba imodzi utha kupeza mma 200k -280k mmamidzimu.Ukachita mwayi kupeza ya 80-100kg ugulitse 15000 per kg
Inu m***a kusankha business idea itiyo pazomwe ndaikazi? Talembani ku comment box tione